Ndalimba Mtima Lyrics
- Genre:Afro Soul
- Year of Release:2024
Lyrics
NDALIMBA MTIMA
Oh oh oh
V1
Chinthu chimodzi ndipempha Yehova
Nkhazikike mnyumba yanuyo
Masiku onse amoyo kuti ndione kukongola kwanu
Moyo wanga ufunisitsa kutumikira dzina lanu
Kwa anthu olengedwa anu kuti adziwe za ufumu wanu
Mtima mwanga ndilakalaka kuphunzitsa za mawu anu Yehova
Kwa anthu amitundu yonse iwo adziwe za mphamvu yanu
Ndipereka moyo wanga kwa inu muugwiritse ntchito Yesu
Anthu anu asimthike iwo adziwe za chikondi chanu
Ine ndalimba mtima kumutsata Mbuye wanga
Zovuta zingachuluke bwanji
Ndatsimikiza sinzamutaya
V2
Ku maiko a nkhondo Yesu chipulumutso chanu chifike
Mawu ponse ponse amasiyenso alimbikitsedwe
Otsekeredwa m’ndende onse mawu anunso awadziwe
Akangamire dzina lanu poti dzina lanu ndilo yankho
Dzetsani chikondi mtima mwanga ku mitima yonse yosweka
Nkaphunzitse za chikndi chanu popeza chilibe malire
Osowa posamira nthawi ya zaovuta
Chikondi chanu sichisankha sichiona nkhope ya munthu
Ine ndalimba mtima kumutsata Mbuye wanga
Zovuta zingachuluke bwanji
Ndatsimikiza sinzamutaya (x3)